Kodi ngati Allah amadziwa zinthu zobisika komanso amadziwa anthu amene adzalowe kumoto ndi ku Paradizo (Jannah) ndi chifukwa chani anatilenga ifeyo?

Question

Ngakhale Allah amadziwa zobisika komanso amadziwa anthu amene adzalowe kumoto ndi ku Jannah panali chifukwa chomwe iyeyo anatilengera nkutiika pa dziko pano. Allah anatilenga kuti adziwike ku zolengedwa zake komanso kuti umodzi wake (Tawhid) utsindikizidwe komanso kuti iyeyo amveredwe. Allah sadzaika anthu ku Jannah kapena kumoto chifukwa chongofuna iyeyo ayi, koma potengera ndi zinthu zomwe munthu amachita padziko pano. Allah akanafuna kuti angoika anthu ku moto ndiku Jannah momwe wafunira zikanatheka ndithu, komano anthu bwezi atayamba kuwona ngati Allah ndi okondera. Ichi ndi chifukwa anatumiza aTumiki ake (Alyhimu-Ssalaam), ma Buku ake komanso kuwapatsa nzeru kuti azitha kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choipa. Dziwani kuti Allah ndi wachilungamo ndipo sasokoneza pakalikonse.